Flames inyamuka ulendo wopita ku Zambia mu masewero opimana mphamvu

Wolemba: Akometsi

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames yanyamuka ulendo wake opita ku Zambia komwe akasewere masewero opimana mphamvu ndi timu ya Chipolopolo ya m’dziko la Zambia.


Timuyi yanyamuka ulendo wakewu kudzera pa bwalo la ndege la Chileka International Airport ku mmawaku.

Timu ya flames ikuyembekezereka kukasewera masewera ake opimana mphamvu ndi a nyamata a timu ya Chipolopolo ku Zambia lachitatu pa 7 October,2020.


Flames ikuyembekezerekanso kudzasewera ndi timu ya Zimbabwe mu masewero opimana mphamvu kumapeto kwa sabatayi.

Anyamata a Flames ndi ena mwa akulukulu pa bwalo la ndege la Chileka.

Masewero onsewa akuchitika ndi cholinga choikonzekeretsa timuyi mu chikho chija cha African Cup of Nations (AFCON) pomwe ikuyembekezereka kudzasewera ndi timu ya dziko lija la Burkina Faso pa masewero omwe adzachitikire kuno ku Malawi komanso kwawo Kwa ku Burkina Faso.

%d bloggers like this: