Untold Stories with Akule: Three Valuable Lessons

Over the weekend, I took a trip to the village to visit my uncle. During my interaction with him, I learnt 3 valuable lessons of life that I simply want to share. That Saturday morning ndinalawira kwambiri ndi cholinga choti ndikabwelere siku lomwelo. I was in the village in good time just as I had planned. By a few minutes past 8 I parked my “bola kuenda chokhala” outside my uncle’s house.

 

I stepped out of the vehicle and made countable steps towards the house when I was welcomed by Huuuu! Huuuu! Huuuuu! The barking and growling of dogs. Thinking of what to do as the dogs continued Huuuu! Huuuu! mayesero othawa anandipeza. Suddenly, I heard a voice of relief, Choka! Choka! it was my uncle chasing the dogs. Anali atavala jekete lawo lokondedwa limene ine ndinayamba kuwaona nalo ndili standard 3. He laughed at me and made funny remarks “galutu amawuwa kwambiri munthu woti sakumudziwa …”

 

Well, that was lesson number 1 for me. You see, in our life there are people who have dog like behaviour. They behave like dogs. They make a lot of noise on things or people they do not know at all. Anthutu oti mwina munangodziwana nawo chifukwa cha ntchito koma amakufotokozani ngati they have known you all your life. They are always the first to present a full report of you, yet they know nothing about you. Don’t be bothered, galu amawuwa munthu wosamudziwa.

 

We greeted each other, he directed that we enter into the house, I quickly suggested that “tingokhala pansi pa ntengo wamangopa bwanji?” He called one of his beautiful daughters (kungoti ndipachibale eti) kuti adzasetse pansi pa ntengowo. Nthawi imeneyo nkuti panali zinyalala komanso miyala yomwe ana amagendera mango muntengomo. Uncle said “mitengo ya zipatso zabwino … monga mango imagendedwa kwambiri … chifukwa anthu amafuna zipatsozo.”

 

Well, that was lesson number 2 for me. You see, ntengo umene umabeleka zipatso zabwino umagendedwa kwambiri. Mupeza pansi pa ntengo wamango, magwafa, mapeyala pali miyala yochuluka koma simuzaona anthu or ana ataunjikana kumagenda ntengo wa Malaina or Bluegum. Yes! such is life. Many a times you will be stoned or go through challenges because of the fruits you are showing. Count it joy when people throw stones at you for what you are. You are showing fruits they will never have, don’t worry akathyola ma fruits amenewo lero mawa you will produce more.

 

Tinakhala pa nthuzi, iwo anakhala pa mpando wawo wa ndalema womwe amaukonda kwambiri. Timamwa thobwa lokoma kwambiri uku tikucheza, nkulu ameneyu amangokholira kuseketsa. Tili nkati mocheza tinangowona mpira wamenya khoma la nyumba ndikubwera mwa liwiro pamene tinakhala ife, pang’onong’ono ukanabudula chigubu cha thobwa lathu. Ana akwa neba anadzatola mpira uja. Malume anangoti “anawa amakonda kuponyera mpira kuno … ine sindidandaula, nyumba yangayi ilibe magalasi … koma siku limene ndizaponyere mpirawu kwaoko magalasi azasweka sure” hahahahahaha!

 

Well, this was lesson number 3 for me. You see, amaponya mpira ku nyumba yoti ilibe magalasi ambiri kuiwala kuti yawo ili ndi magalasi ochuluka zedi. Moyonso ndichoncho ndithu, alekeni aziponyera mpira kunyumba yanuyo uzingomenya khoma basi. Inu mukazaponya kamodzi kapena kawiri kokha magalasi anyumba yawoyo azayoyoka koopsa. Ndimoyo uwu!

%d bloggers like this: