Untold Stories: Asset declaration

Good morning! the recent judgement by Judge Sylevester Kalembera’s ruling says “degrees, professional licences, or any other qualification that a person obtains while married belong to both the husband and wife”. The learned judge made these observations pamene amaweluza nkhani ya banja lina lomwe linayamba mchaka cha 1995 ndipo linatha nchaka cha 2012.

Anthuwa ali pa banja bambo amapangabe school nkupeza ma qualifications ena. In all fairness, some people are happy with this ruling others have embraced it with somberness. This is a ground breaking case and I strongly feel the implications of this ruling are sensitive, we have to swallow our pride and tread carefully in this new reality. From my little understanding, this protects both parties; the man and the woman.

Yesterday I was watching Bayana Chunga’s Spotlight on Times Television where they were discussing the same issue. Bayana shared this story, akuti kumene ankakhala kunali bambo wina amene anapita ku Bunda kukaonjezera maphunziro. Ndie nkulu ameneyi anauza nkazi wake kuti chifukwa choti ndili ku school zinthu zizitivuta pakhomo pano, bwanji mupite kaye kumudzi sukuluyi ikatha ndizakutengani.

Anamaliza school kuyamba ntchito mmalo mokatenga madam kumudzi anakwatira nkazi wina. Wakumudzi uja atamva anabwera mokwiya kwambiri phopholali nyumba yonse magalasi, chinam’balala pakhomo ponse zionetselo zokwiya mzimayi, zinachita kutengera a polisi kuzakhazikitsa bata. Nthawi zambiri anthu akakhala pamwamba amaiwala makwelero amene anagwiritsa ntchito kuti afike pamenepo.

Ubwenzi wankhwanga wokoma pokwera. Kumudzi kwathu kunali nkamwini dzina lake Mwandiyambadala, anali wozilimbikira ndithu. Anamanga nyumba yake ya malata, anaswa mphanje ndikutsegula munda komanso madimba. Atangopanga zimenezo basitu banja yambani kuvuta akazi ake akuti “muzipita sindikukufunaninso pano … useless man.”

Mwandiyambadala sanavutike, pochoka anasatsula malata anyumba yake, ma frame azitseko ndi mawindo hahahahahaha! Inalinso nthawi yoti chimanga chili mmunda chayamba kumene kumasula, nkamwiniyu anabwera usiku kuzatchetcha chimanga munda wonse. Ameneyudi koma anamuyamba dala.

Mantha anga pa umunthu is that this ruling seems to commercialise marriages. Kodi munthu azilowa m’banja ndicholinga choti akapindulemo interms of finances or property? Food for thought. Look at this, pa 26 August chaka chomwechino Annie Mumba the wife of late Proffessor Peter Mumba who was a lecture at Bunda University anamangidwa poganizilidwa kuti anapha amuna awo kuti atengechuma.

Judge chigamulo tachimva koma munanaiwalanso passport, passport ikhalenso family property makamaka anthu oyenda ku Joni. Amavutika ndi akazi kulima mpunga, fodya, ndi chimanga basi akapita uko kukakwatira mazulu hahahahaha! chipongwe chachikulu.

Assert declaration polowa m’banja basi, “inetu ndikulowa m’banjamu ndili ndi JCE, njinga, mphatsa, ndi nsuko … nanga iwe mnzanga wabwera ndi chani?” ndie winayonso afotokoze zimene wabwera nazo, chonchobe a Malawi tizolowera.

Untold stories ….. end times are here eeeeeeeh

 

Akule Chikopa

%d bloggers like this: