Thupi la “Ambuye Yesu” labedwa ku Mangochi diocese

Akometsi.

 

Thupi lomwe a khristu a chikatolika amakhulupilira kuti ndi la Ambuye Yesu, linabedwa ndi akuba ku Parish ya Kamkao m’boma la Balaka yomwe ili mu diocese ya Mangochi la mulungu pa 30 August, 2020.

Malingana ndi chikalata chomwe chinasainidwa ndi m’busa Montfort Stima, thupilo linabedwa pamodzi ndikatundu wina monga ma laptop, zikwama ndinso ndalama.

Pakutsatira izi, Stima wauza akhristu onse a chikatolika kuti achite mapemphero apadera otchedwa ‘Novena’ omwe adzayambe pa 14 September chaka chomwe chino.

Mukuyankhula kwake, Stima adapempha a nsembe ndinso ma sisiteli kuti ayambe mapempherowa pa 7 September, 2020yomwenso ndi nyengo yomwe akhristu a chikatolikaamapempha chikhululuko kwa Ambuye Yesu m’Khristundikutinso mbavazo zigwidwe.

Poonjezerapo, iye adapemphanso a khristu a chikatolika kuti apitilize kupemphelera ma sisiteli a pa Poverelle Kankao parish pamene akudutsa mu nyengo za mayesero.

Aka ndi koyamba mu mbiri kuti akuba athyole tchalitchi ndikuba thupi la Ambuye Yesu.

%d bloggers like this: