Zabwino Zawo ndi Zofowoka Zawo – Bambo Saulos Chilima

Bambo Saulos Klaus Chilima anabadwa pa 12 February chaka cha 1973 ku Ntcheu. Iwo ndi Vice President wa Malawi pakadali pano komanso president wa UTM.

Sukulu yawo anapanga ku Marist Brothers ku Dedza kenako nkusankhidwa kukapanga ukachenjede oyendetsa za chuma ku Chancellor College komwe anapangakoso Masters Degree. Iwo analandiranso Ph.D in Knowlegde Management ku Bolton University yaku England.

Bambo Chilima anagwirako ntchito zosiyana siyana ku Sobo komanso anali bwana wankulu ku Airtel Malawi pomwe amayamba ndale ndikukhala Vice President wa Malawi.

Mwachidule titere:

Zofowoka Zawo

1. Amawopseza anthu ochita katangale kuti adzamangidwa
2. Amakonda kunyaditsa za thanzi lawo pa misonkhano popanga ma push ups ndi zina zotero
3. Sapuma kweni kweni akayamba kugwira ntchito
4. Amadziyamikira kuti amaganiza bho heavy zomwe zimawonekadi kuti ndizowona

Zabwino Zawo

1. Ndiwophunzira bwino komanso ophunzitsidwa kwathu konkuno
2. Olimbikira ntchito kwambiri
3. Wachinyamata ma looks pompo, plus kuganiza bho kuja
4. Amakondedwa ndi chigulu kuyambira ku mudzi ndi mtowni momwe
5. Amatha kuyanjanitsa anthu mkugwira ntchito pamodzi molimbika
6. Amadana ndi katangale ndipo amanenetsa kuti adzatha ndi onse akatangale
7. Amadziwa kukhala ndi anthu ndipo amalimbikitsa moyo olimbikira ntchito
8. Ndi munthu oti wadzichitira zambiri payekha osadalira Adad
9. Wapereka chilimbikitso kwa achinyamata ambiri
10. Sachita nawo zombwambwana
11. Amakhala committed ku chinthu akayamba
12. Amakonda kupemphera
13. Amalemekeza mamfumu ndi a chipembedzo
14. Sanaluzeko mlandu
15. Ndiye anabweretsa mfundo ya feteleza otsika mtengo zomwe zakondweretsa Malawi

Izi ndi zina mwazabwino ndizofowoka za Bambo Chilima. Zikomo Akometsi.

%d bloggers like this: