Zabwino Zawo ndi Zofowoka Zawo – Bambo Peter Mutharika

Bambo Peter Mutharika yemwe ndi President wa Malawi pakadali pano ali ndi zaka 79 poti anabadwa mu chala cha 1940 ku Malawi.

Za mbili ya kuumwana wawo siyipezeka kweni kweni koma iwo adapanga ukachenjede wa maphunziro awo ku sukulu ya pamwamba kwambiri ya Yale University ku America komwe adzaphuzirako ukadaulo waza malamulo (Law).

Bambo Mutharika aphuzitsakonso ma University osiyana siyana monga University of Dar es Salaam ku Tanzania, University of Haile Selassie ku Ethiopia, Rutgers University and Washington University ku USA ndipo anakhalakonso mlangizi waku American Bar Association’s Rule of Law Initiative in Africa.

Kuno ku Malawi pomwe malemu mkulu wawo Bingu Wa Mutharika anakhala president, iwo anayitanidwa kudzamuthandiza kuyendetsa dziko ndipo anakhalako nduna yaza Maphunziro komanso nduna yowona nkhani za kunja ndinso nduna yaza Malamulo.

Mwachidule, tiyeni titere:

Zabwino Zawo

1. Ndiwophunzira kwambiri
2. Ndi mphwawo wa Malemu Bingu Wa Mutharika
3. Alibe nkhanza zokonda kumanga a ndale anzawo
4. Anakulira kunja
5. Samwa Kachasu koma Vinyo
6. Ali ndi mtima ofuna kutukula Malawi kufika pa Singapore  ndi America

Zofowoka Zawo

1. Amawoneka kuti zochita mu dziko mwathumu siziwakhudza kweni kweni
2. Amasowa ku gulu kwa anthu, campaign angopanga masiku owerengeka komanso ku mpoto apitako kamodzi pa miyezi khumi ndi iwili.
3. Kuyankhula Chichewa kugulu satha kweni kweni kamba kokulira kunja
4. Sagwirizana ndizogamula court zikapanda kuwakomera. Amalusa kwambiri
5. Boma lawo limatchuka ndi tsankho lokondera mtundu umodzi malinga ndi mene amapangira apoint maudindo akulu akulu ndiso ndikalembedwe ka ntchito ka anthu m’boma
6. Ndiwachikulire kwambiri ofunika kupuma. Ali ndi zaka 79 komanso agwira ntchito nthawi yayitali
7. Sachedwa kuyiwala poyankhula, amatha kuyiwala ngakhale capital city ya Malawi
8. Boma lawo limatchuka ndikuika miyala yamaziko komanso malonjezo osakwanilitsidwa monga Mombera University ndi misewu yambiri yomwe ndalama zake zimatuluka chaka ndi chaka mu budget ya dziko lino koma osamanga
9. Boma lawo limadziwika kwambiri ndima fuel allowances ankhani nkhani
10. Kwatuluka nkhani za corruption zambiri mu nthawi yomwe akhala president wa dziko

Izi ndi zina mwazabwino komanso zofowoka za a Peter Mutharika amene akuimira mgwirizano wa DPP ndi UDF pazisankho zikupangidwa mawazi. Zikomo Akometsi.

%d bloggers like this: