Zabwino Zawo ndi Zofowoka Zawo – Bambo Lazarus Chakwera

Bambo Lazarus McCarthy Chakwera ndi m’tsogoleri wa chipani cha MCP amenenso akuimilira Tonse Alliance pa zisankho za chibwereza zosankhanso president wa dziko lino.

Iwo anabadwa mu chaka cha 1955 pa 5 April ku Lilongwe ndipo ndi mwamuna yekhayo amene anatsala pa ana obadwa m’banja mwawo.

Bambo Chakwera anapanga maphunziro awo aukachenjede ku Chancellor College ya University of Malawi komwe anachokako ndi degree ya Arts (Philosophy). Iwo analandiranso ma degree ena aukadaulo ku South Africa komanso ku USA.

Tikatengera maphunziro awo, a Chakwera ndi ‘Professor’ koma sakondwa kutchulidwa kuti Professor kapena kuwatamandira kwambiri za sukulu yawo. Iwo amati ndi mtumiki wa anthu chabe basi.

A Chakwera adayamba ndale mu chaka cha 2013 pomwe anamva kuitanidwa kudzatumikira dzikoli ndi ambuye. Ulendo wawo wakhala wachiphunzitso chakuya komanso onyaditsa malinga mkuti zomwe ambuye anawayitanira zatsala ma ola ochepa kuti zitheke.

Mwachidule, tiyeni tiwafotokoze motere:

Zofowoka Zawo

 1. Amayankhula moleza mtima
 2. Sanatukwaneko munthu pa msonkhano
 3. Amayankhula chizungu chokhotetsa lilime chaku America
 4. Sakwiya kwiya. Pomwe akwiyila ndiye kuti zavutitsitsa
 5. Samwa Kachasu olo Vinyo

Zabwino Zawo

 1. Ndiwophunzira kwambiri
 2. Amawopa Mulungu ndinso kuphunzitsa anthu za ubwino wa Mulungu
 3. Ndi munthu olemekezeka komanso okonda banja lawo
 4. Sadzikundikira chuma
 5. Amalimbikitsa Servant Leadership. Utumiki otumikira anthu mosadzitukumula
 6. Anasintha MCP, kuchoka pa mbiri ya nkhanza kufika pa mbiri yokomera aliyense mosayang’ana mtundu
 7. Ali ndi nzeru zachikhalire zoyendetsa zinthu modekha
 8. Mulungu amawakonda, anthu ayesetsa kufuna kuwagwetsa koma zakanika
 9. Amagwirizana kwambiri ndi Chilima ndipo amakondana
 10. Alibe mbiri yakatangale ndipo nkhani za ndalama amayendetsa bwino kwambiri
 11. Amachita ntchito zambiri zachifundo mosadzitukumula. Mwa zina, iwo amalipilira anthu ma school fees ndizina zambiri
 12. Ndiwovetsetsa pa zinthu ndipo amakonda mtendere

Amene amakhala nawo pafupi amayikira umboni ndithu kuti a Chakwera ndi munthu wama principles abwino ndipo alibe mtima ofuna kungowatola ena mkuwagwiritsa ntchito. Ndi mtsogoleri omvetsetsa komanso okonda anthu omwe akuwatumikira. Zikomo Akometsi.

%d bloggers like this: