Zabwino Zawo ndi Zofowoka Zawo – Bambo Atupele Muluzi

Bambo Atupele Muluzi anabadwa m’chaka cha 1978 pa 6 August ku chipitala cha Kamuzu Central Hospital ku Lilongwe.

Nthawi yomwe iwo amabadwa ndipo kuti abambo awo a Bakili Muluzi ali m’modzi mwa mamulumuzana akulu akulu achipani cha Malawi Congress Party. Ndi magulu aja amayendetsa za ma card mkumakutumula anthu osadula card la chipani.

Mwachidule, iwo ndi mwana yemwe anakula moyo wabwino kwambiri, kuphunzira ma school apamwamba komanso kupeza chuma cha nkhani nkhani chomwe bambo awo anapanga pa nthawi yomwe anali president.

Bambo Atupele adaphuzira sukulu yawo yaku umwana ku Eastridge ku Zimbabwe, S.T Andrews International High School ku Malawi, Bentham Grammar School ku Yorkshire ku Mangalande. Za ukachenjede zawo anapangira ku University of Leicester ku Mangalande komweko komwe adaphunzira ukadaulo waza malamulo (Lawyer).

Mavuto eni eni achimalawi sawadziwa poti iwo sanakule ngati m’Malawi weni weni. Mwa zina, bambo Atupele Muluzi sanakuse nawo ng’ombe, sanayendetseko galimoto za dongo, kusambira anaphuzilira mu swimming pool osati mu m’tsinje, mbuluwuli sazidziwa, likhwelu lobweza ng’ombe zikasochera sangaimbe, ntchito la botolo la Covo masiku amene popita ku sukulu sayidziwa. Iwo koma muwafuse za ma sausage, play station, channel O, business class, Cinema, pocket money ya ngati salary ndizizake.

Mwachidule, tiyeni titere;

Ubwino Wawo

1. Ndi mwana wa Mtsogoleri wakale
2. Anakula moyo ofewa
3. Amakonda abambo awo kwambiri
4. Ali ndi ulemu kwa akulu akulu
5. Anakhalapo Minister kangapo maboma osiyana siyana
6. Ndende amayidziwa. Anadwalapo blood pressure atangokhala ku cell for 2 hours pomwe anamangidwa ndi boma la DPP
7. Anaphunzira experience yoyendetsa dziko kwa abambo awo
8. Ali ndi ma connection ambiri kunja kwa dziko lino moti ngakhale president waku China amawayitana kukacheza nawo
9. Ndi munthu odziwa malamulo
10. Ndi wa chinyamata

Zofowoka Zawo

1. Amakonda maudindo kwambiri
2. Ali ndi dyera la kubanja kwawo lomwe limawapangitsa kusaganizira kwambiri za a Malawi
3. Mfundo alibe, tamva tonse mayankhulidwe awo pomwe abali pa campaign amayankhula zoduka mutu
4. Amadalira a bambo awo zikavuta ndipo sapanga chinthu opanda nzeru za bambo awo
5. Mavuto sawadziwa akulira pa chinena (izi takamba kale)
6. Adalephera kangapo mayeso oti azipanga za u lawyer m’Malawi muno (Bar Exams)
9. Kwawo komwe ku Machinga sawafuna mpaka sadawine u MP mu 2019
10. Ali ngati stock margarine pakati pa a Adad awo a ndale a Peter Mutharika ndi Adad awo owabereka a Bakili Muluzi.

Izi ndi zina mwazofowoka komanso ubwino wa bambo Atupele Muluzi. Zikomo Akometsi

%d bloggers like this: